
Anthu amene akuchita maphunziro komanso alindikhumbo lochita maphunziro a utolankhani akuyenera akonzeke mokwanila pamene sukulu yosula atolankhani ya Malawi Institute of Journalism( MIJ) yakweza ndalama yolipilira maphunziro pa sukuluyi kuyambira January 2027.
Kudzera mu kalata yomwe sukuluyi yatulutsa lero yati ndalama ya ophunzira omwe akuchita apamwamba a digiri yakwera kuchoka pa K500,000 pa semisita kufika pa K700,000 kutanthauza kuti pachaka azilipila ndalama zokwana K1,400,000 kuchoka pa K1,000,000.
Fizi ya omwe akuchita dipuloma, ayamba kulipira K600,000 pa semisita kuchoka pa K400,000 pa semisita ndipo pachaka azilipira K1,200,000 kuchoka pa K800,000.
Izi zikudza pomwe sukulu za ukachenjede za boma zinakweza fizi ndi 100 Kwacha pa 100 Kwacha iliyonse posachedwapa, kuyambira mu chaka cha 2026/2027 chomwe chinayamba mu September 2026.



