
Mpungu wa nyumba ya malamulo oima payekha yemwe ndi wachipani chotsutsa boma cha Malawi Congress Party kuyambila kale , a Sylvester Ayuba James awuza mlembi wamkulu wa chipanichi a Richard Chimwendo Banda kuti iwo ndi anthu ena omwe amadzudzula chipanichi pazolakwika zina sakutuluka chipanichi kukalowa china or kuyambitsa china momwe a Chimwendo Banda anayankhulira ponena kuti chipanichi sichamawo.
Ayuba analemba izi patsamba lamchezo la Facebook;
Sitikupita kulikonse mafana. Tili mu MCP momwemu. Chipani anayambitsa ndi anthu a ku mpoto ichi. Inunslkapena tikalowa china, mwauponda. We are not going anywhere.
If you insist on your path of disgrace, ife 2030 todzakhalabe osangalala because we will be vindicated. Tidzakhala tikuseka koma moyo wathu ukuyendabe bwino, inu m’boma mutalephera kubwerera.
We are not going to lose anything at all, koma chipani sitingachisiye chifukwa si cha amanu. Chifukwa chabe cha ubulutu mumaona ngati chipani ichi anayambitsa ndi makolo anu. Kawerengeni mbiri ya dziko lino ngati mumamva chizungu.



