
Sheikh Hashim Abbas omwe anali wachiwiri kwa mlangizi wa mtsogoleri wakale wa dziko lino a Lazarus Lazarus Chakwera pa nkhani za chipembedzo amwalira.
Sheikh Abbas amwalira akulandira thandizo la chipatala lero pa chipatala cha Kamuzu mu nzinda wa Lilongwe.
Mchaka cha 2025 Sheikh Abbas anapikisana nawonso pa chisankho pa udindo wa phungu wa nyumba ya malamulo m’dera la Zomba Mtonya.
Thupi lalemu Sheikh Abbas likuyembekezeleka kuikidwa mmanda mawa lachitatu pa 14 October 2026, mmudzi wa chipande, m’dera la mfumu yayikulu Chikowi m’boma la Zomba.



