
Galimoto lomwe linabedwa ku nyumba kwa wansembe wa mpingo wa Katolika mu Parishi ya St. Lawrence Nkoka ku Blantyre yapezeka.
Malipoti ati galimotoli lapezeka ku Soche kwa Manje m’mawa uno koma mbavazo sizinapezeke.
Bambo George Buleya omwe ndi Vicar General wa arkidayosizi ya Blantyre bambo atsimikiza kuti galimotoyo ndi lomwelo.
Pakadali pano, galimotoyo alitengera ku polisi ya Manase komwe akufufuza zambiri zokhudza kubedwa kwa galimotoyo ndi katundu wina monga kompyuta, lamya za m’manja ndi katundu wina yemwe anasowa



