
Apolisi ku Euthini Pansi pa Polisi ya Kafukule amanga bambo wazaka 23 aJohn Kachali powaganizira kuti amasunga mfuti Shuangwe I.C.18 ya mtumdu wa pistol yopanda zipolopolo popanda chilolezo yomwe amagwiritsa ntchito poopsezera mkazi wawo.
Mneneri wa polisi ya Kafukule Thomas Jemitala, wati Kachali wamangidwa pa 25 September 2026 mkazi wake atakanena ku polisi kuti Kachali anapeleka mfutiyi kwa mkazi wake wachiwiri ndikumuuza kuti aziwopsezera mkazi wake oyamba pa nthawi ya mkangano wa awiriwa.
Jemitala wati apa apolisi anakachita chipikicheni ku nyumba ya oganizilidwayu limodzi ndi nkuluyu komwe anakapeza mfuti ya mtundu wa pistol yopanda zipolopolo.
Kachali amakhara m’dziko la South Africa ndipo anabwelera mdziko muno mu mwezi wa June 2026 ndi katundu wake kuphatikizapo mfutiyi yomwe akuti abwana ake anamupatsa ngati yodzitetezera.



