Pomwe kuli khwimbi la mundipondela mwana pa bwalo lamasewero la Sukulu ya Pulayimale ya Malembo, pomwe phungu wa dera la Lilongwe Chilobwe, a Lawrence Chakakala Chaziya, akuchititsa msonkhano wa ndale.
Aphungu a chipani chotsutsa cha Malawi Congress Party (MCP) oposa khumi ochokera m’madera osiyanasiyana omwe ali nawo pa msonkhanowu, ati akufuna mtsogoleri wakale wa dziko lino, yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha MCP, a Lazarus Chakwera, adzayimile chipanichi mu masankho a 2030.
Aphungu onse omwe ali pamsonkhanowu ati mtsogoleri wa chipanichi, a Lazarus Chakwera, akufunidwa kuti adzayimilenso mchaka cha 2030 ndi anthu ambiri m’madera awo.
“Anthu m’madera athu akuti akufuna a Chakwera adzayimilenso mu 2030, ndipo tati a Malawi mudziwe zimenezi,” atero aphungu angapo.
Ena mwa aphunguwa adzudzulanso boma lolamula la DPP chifukwa chosaganizira mavuto ena omwe a Malawi akukumana nawo.
“Inde chimanga chikupezeka ndipo chakudya sichikusowa, koma a Malawi ali ndi mavuto ambiri,” anatero a Chaziya.
Mwa zina, aphunguwa anadandaula za kukwera kwa mitengo ya feteleza, kukwera kwa fizi m’makoleji, mitengo yotsika ya mbewu, ndi mavuto ena.
Aphungu enanso anati boma mwina lichepetse ndalama za CDF kufika pa mulingo umene lingakwanitse, chifukwa pakali pano palibe chilipo.