
Phungu wa dera la pakati pa boma la Nkhotakota Ayuba James yemwenso ndi membala wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP), wati zomwe amayankhula mlembi wa chipani cha MCP a Richard Chimwendo Banda m’misonkhano, akanakhala kuti amayankhula mmadera ena bwezi ataona nsana wanjira ndi miyala komanso kuwowozedwa.
A James ati ndi zotsadabwitsa kuti misonkhano yawo ikungozungulira pa Malirana Turn-off ndi Chatoloma.
Iwo ati zomwe akumayankhula mlembiyu ndi zopanda pake, chikoka komanso uthenga osowa chokuti munthu atha kutenga ndi kukalingalira kunyumba.
“Pali mwayi ochuluka omwe angathe kugwilitsa ntchito kukopa anthu kudzera pa momwe zinthu zikuyendera mdziko muno ndi zomwe MCP yaphunzira koma chomwe akuchita ndi kuzikweza”.
“Padzana ku Dowa kuwukunga mtudzu kuti amene safuna Chakwera achoke. Verbatim. Aliyense akumva. Dzulo ku Ntchisi, after receiving a backlash from all quarters except a handful of fellow zealots, waitembenula. Akuti “ine ndinanena kuti amene mukufuna kuchoka muchoke mwa mtendere”.
Iwo ati a Chimwendo amaganiza kuti aliyense ndi kaganizidwe kamomwe amaganizira kuiwala kuti pali anthu ena oganiza mwanzeru kusatengera kuti anamwetsedwa maheu.
A James ati ndi zomwe akuyankhula a Chimwendo asamadabwe kuti anthu akumatukwana mtsogoleri wachipanichi kuti samatha ntchito.



