Phungu wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP), a Lawrence Chaziya, adzudzula ganizo la mtsogoleri wa chipanichi, a Lazarus Chakwera, lofuna kuti anthu omwe akufuna maudindo osiyanasiyana m’chipanichi azipereka ndalama potengera udindo womwe akufuna kupikisana nawo.
Polankhula kwa Nsundwe pa mwambo wokhazikitsa mbendera womwe unakonzedwa ndi phungu wa ku Delari, a Edwin Chileka Banda, a Chaziya ati ganizo lofuna kuti munthu azipereka ndalama malinga ndi udindo womwe akufuna kupikisana nawo silikumveka ndipo sangagwilizane nalo.
Ganizoli linabwera pambuyo poti akuluakulu a MCP akambirana za momwe chipanichi chingapezere ndalama zokwana K2.5 biliyoni kuti chisankho cha mkati mwa chipani chitheke m’zigawo zonse za dziko, kuyambira ku Nsanje mpaka ku Chitipa.
Pakadali pano, otsatira MCP omwe analipo pamsonkhanowo akuyembekezera kumva maganizo a a Jessie Kabwira pa zomwe a Chaziya ananena.
Izi zikuchokera pa mfundo yakuti pa tsiku lomwe ganizo lokhudza kulipira ndalama kwa anthu ofuna maudindo linakambidwa, a Kabwira analiponso koma sananene chilichonse panthawiyo.
Ena mwa otsatirawo akufunsa ngati a Kabwira apereka maganizo awo pa nkhaniyi, makamaka poganizira kuti akuti akufuna udindo wa mlembi wamkulu wa chipanichi, womwe pakadali pano uli m’manja mwa a Richard Chimwendo Banda.