
Bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) latseka malo omwetsera mafuta a Mount Meru kwa Chinsapo ku Lilongwe zitadziwika kuti malowa anasunga mafuta okwana malita 1,000 kuti agulitse kwa anthu ena osankhika pokanidza anthu ena kugula mafutawa.
Malingana ndi chikalata chomwe bungweli latulutsa lero yati malowa adzatsekulidwanso mtsogolomu.
Izi zikudza pamene vuto lakusowa kwa mafuta a galimoto dziko muno likupitilirabe.
Masiku apitawa bungweli lakhazikitsa njira zoti ati anthu azinenedza mchitudwe wogulitsa mafuta mwachinyengo ndipo azapatsidwa mphoto pamapeto pake.
Nkhaniyi yabweletsa nsutso pakati pa a Malawi omwe akuti bungweli likanangopanga zoti mafuta azipezeka mosavuta yomwe ndi njira yokhazikika yothanilana ndi mchitidwe wogulitsa mafuta mwachinyengo osati zopeleka mphoto zomwe akhazikitsazo.
j