
Timu ya Ekhaya yachotsa ntchito mphunzitsi wake Enos Chatama.
Malingana ndi kalata yomwe wasayinira ndi mkulu watimuyi, Thando Mhango, atawunikira zomwe akufuna kukwanilitsa kutsogoloku.
Kalatayi yathokozanso a Chatapa kamba kakuizipeleka kwawo komanso zimene apangira timuyi pa nthawi imene iwo anali ku timuyi.
Pakadali pano, wachiwiri kwa mphunzitsi Fundi Akidu ndiyemwe akhale mphunzitsi ogwirizira mothandizidwa ndi Moses Chavula.
Izi zikudza patangopita sabata ziwiri timuyi itatenga chikho cha Airtel Top 8. Ekhaya yamaliza gawo loyamba la FDH Bank Premiership polepherana ndi Karonga United 0-0.