
Patangotha maola ochepa timu ya Ekhaya italengeza kuti yasiyana ndi Mphunzitsi wake wamkulu Enos Chatama, Usiku wapitawu timu ya Silver Strikers yalengedzanso kuti yalekana ndi Peter Mgangira yemwe anali Mphunzitsi wamkulu wa timuyi.
Malingana ndi kalata yomwe timuyi yatulutsa kuchotsedwa kwa a Mgangira ndi kaamba ka mmene timuyi ikuchitira mmasewero ake.
Mgangira akuchosedwa patangotha masiku ochepa chabe timuyi itasambitsidwa mtibu wazigoli zisanu kwa duu ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets mu masewero ake omali a gawo loyamba la ligi ya FDH Bank Premiership.
Silver Strikers yakhala timu yachitatu kusiyana ndi mphunzitsi wamkulu kusatila Mighty Wanderers yomwe inayimitsa kaye Bob Mpinganjira ndi Ekhaya FC yomwe yachotsa ntchito Enos Chatama.