
A Getrude Muliko azaka 48 omwe ndi amudzi mwa Mulolo m’dera la mfumu yayikulu Mulolo m’boma la Nsanje ndipo amagwira azaumoyo m’boma la Ntcheu adzipha pozimangilira mnyumba mwao.
Malingana ndi wofalisa nkhani za Polisi ya Ntcheu a Jacob Khembo, panthawi yomwe mayi Getrude amadzipha mwana wawo wazaka zisanu ndi ziwiri anali akuona ndipo amalira kwambiri zomwe zinapangitsa anthu ozungulira kuthamangira ku nyumbayo.
Khembo wati anthuwo atafika mnyumbamo anapeza kuti mayiwo adzimagilira.
Iye wati padakali pano thupi la mayi Getrude Muliko lili kunyumba yachisoni pachipatala cha Ntcheu kudikilira kuti alipime.
Malingana ndi wofalisa nkhani za polisi yu imfa ya mayi Muliko ndi yachitatu musabata ziwiri yomwe anthu m’bomali akudzipha ndipo apempha anthu kuti aleke mchitidwewu ndikumapempha nthandizo loyenela kwa adindo ndi anthu ena.



