
Wofalitsa nkhani za Polisi ya Mzuzu, a Cecelia Mfune watsimikiza zoti apolisi akusaka bambo wina Overstone Soko pomuaganizira kuti adathyola khosi mpaka kuphelatu mayi Kestina Kumwenda omwe adali nawo pa ubwenzi.
Mfune wati kuti thupi la a Kestina Kumwenda, omwe akuganizilidwa kuti adaphedwa masiku apitawa lidapezeka litayamba kuwonongeka mu nkhalango ya Chandamale kumalo amene a Soko ankagwirako ntchito yowotcha makala.
Malipoti akuwonetsa kuti a Soko adapha mayi Kumwenda kaamba koti adathetsa ubwenzi wa awiriwa pamene adachita ganizo lofuna kubwelerana ndi amuna awo akale zimene zikuowonetsa kuti bamboyu sanakondwele nazo.



