Skip to content

Malawi Cables Online

We Report the Future — the Only Trusted Source of News with a Difference

Primary Menu
  • Home
  • Latest
  • News
  • Breaking News
  • Religion
  • Economics
  • Politics
  • Sports
  • Home
  • Blog
  • Home
  • Latest
  • CAMA YATI BOMA LITHETSE MISIKA YOSAVOMELEZEKA (BLACK MARKET) YA MAFUTA AGALIMOTO KOMANSO KUTHANA NDI VUTO LAKUSOWA KWA GASI
  • Latest

CAMA YATI BOMA LITHETSE MISIKA YOSAVOMELEZEKA (BLACK MARKET) YA MAFUTA AGALIMOTO KOMANSO KUTHANA NDI VUTO LAKUSOWA KWA GASI

Andy Ten October 18, 2026 (Last updated: October 18, 2026)

Mkulu wa bungwe la Consumers Association of Malawi (CAMA), a John Kapito wauza boma kuti lichite changu kuthetsa vuto lakusowa kwa mafuta a galimoto ndi gasi m’dziko muno.

Polankhula lero pa msonkhano wa atolankhani ku Blantyre a John Kapito ati nzodandaulitsa kuti msika wa mafuta a galimoto wachinyengo (black market) ukukula mdziko muno.

A Kapito ati boma lithetse msikawu popereka ziphaso ku kampani zambiri kuti zizibweretsa mafuta a galimoto mdziko muno.

Mkulu wa CAMA yu wati ndizodandaulitsa kuti anthu akugona ku malo omwetsera mafuta ndipo ena akukakamizika kugula pa mtengo wa K15,000 pa lita.

Iwo ati boma lisiye kupereka ndalama za kunja (forex), kuti anthu adzigula galimoto ndi kuti ndalamazo agwiritse ntchito kugulira mafuta a galimoto.

A Kapito omwe anali limodzi ndi akuluakulu a kampani yogulitsa gasi ya Gasman pa msonkhanowu apempha boma kuti kwapano boma ilole kampani zogulitsa gasi kuti zidzigulitsa pamtengo umene angafune.

Akuluakuluwa ati izi zitha kuthandiza kuti gasi apezeke mosavuta m’dziko muno pano pomwe wakhala akusowa kwa pafupifupi miyezi itatu tsopano.

A Mark Wheeler aku Gasman ati vuto la gasi lakula chifukwa chakusowa kwa ndalama zakunja.

“Ku South Africa komwe timagula gasi alipo ochuluka chomwe chikuvuta ndikusowa kwa ndalama zakunja,” anatero Wheeler.

Mkuluyu watinso bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) ilole ma kampani kumagulitsa gasi pa mitengo yosiyanasiyana.

“Tikanakonda MERA isiye kaye kukakamiza kuti tizigulitsa pa mtengo umodzi,” watelo Wheeler.

Pomaliza a John Kapito anati kulekelera mavutowa zipangitsa kuti kampani zina azitseke zomwe zipangitse kuti anthu ena akhale pa ulova m’dziko muno.

About the Author

Andy Ten

Editor

Journalist from Mangochi former student and University of Malawi, The Polytechnic

View All Posts

Like this:

Like Loading…

Related

Post navigation

Previous: Mkulu Wina Akusakidwa Ndi Apolisi Kaamba Kothyola Khosi Ndi Kupha Bwenzi Lake
Next: A SECURITY GUARD KILLED BY THUGS IN BALAKA

Related Stories

6b2338e4-24a1-4960-80a5-06d6d6abc48b
  • Latest

NICO Group Pledges Continued Support To Preserve Malawi’s Cultural Heritage at Mulhako wa Alhomwe 2026

Malawi Cables October 18, 2026
1000128418
  • Latest

A SECURITY GUARD KILLED BY THUGS IN BALAKA

Andy Ten October 18, 2026
1000127373
  • Latest

Mkulu Wina Akusakidwa Ndi Apolisi Kaamba Kothyola Khosi Ndi Kupha Bwenzi Lake

Andy Ten October 18, 2026

Recent Posts

  • NICO Group Pledges Continued Support To Preserve Malawi’s Cultural Heritage at Mulhako wa Alhomwe 2026
  • A SECURITY GUARD KILLED BY THUGS IN BALAKA
  • CAMA YATI BOMA LITHETSE MISIKA YOSAVOMELEZEKA (BLACK MARKET) YA MAFUTA AGALIMOTO KOMANSO KUTHANA NDI VUTO LAKUSOWA KWA GASI
  • Mkulu Wina Akusakidwa Ndi Apolisi Kaamba Kothyola Khosi Ndi Kupha Bwenzi Lake
  • APM IS STILL GOVERNING MALAWI: A PRIVATE TRIP DOES NOT MEAN THE COUNTRY HAS STOPPED

Recent Comments

No comments to show.

Archives

  • October 2026
  • September 2026
  • August 2026
  • July 2026
  • June 2026
  • May 2026
  • April 2026
  • March 2026
  • February 2026
  • January 2026
  • December 2025

Categories

  • Breaking News
  • Economics
  • Home
  • Latest
  • News
  • Politics
  • Religion
  • Sports

You May Have Missed

6b2338e4-24a1-4960-80a5-06d6d6abc48b
  • Latest

NICO Group Pledges Continued Support To Preserve Malawi’s Cultural Heritage at Mulhako wa Alhomwe 2026

Malawi Cables October 18, 2026
1000128418
  • Latest

A SECURITY GUARD KILLED BY THUGS IN BALAKA

Andy Ten October 18, 2026
1000127522
  • Latest

CAMA YATI BOMA LITHETSE MISIKA YOSAVOMELEZEKA (BLACK MARKET) YA MAFUTA AGALIMOTO KOMANSO KUTHANA NDI VUTO LAKUSOWA KWA GASI

Andy Ten October 18, 2026
1000127373
  • Latest

Mkulu Wina Akusakidwa Ndi Apolisi Kaamba Kothyola Khosi Ndi Kupha Bwenzi Lake

Andy Ten October 18, 2026
Copyright © 2026 All rights reserved. | ReviewNews by AF themes.
%d