
Apolisi m’boma la Lilongwe amanga amayi atatu powaganizira kuti anabisa kubadwa kwa mwana komanso kumuponya mumtsinje wa Lilongwe, m’dera la Mgubo, ku Chiwamba.
Mneneri wa apolisi a ku Kanengo, Sub Inspector Macfarlen Mseteka, amayi atatuwo ndi a Ivy Lyson azaka 26, a Mulitani Chotsani azaka 31, komanso a Mary Santhe azaka 40, onse ochokera m’mudzi wa Mgubo, kwa Mfumu Yaikulu Chimutu.
Apolisi ati pa 1 November 2026, anthu a m’deralo anapeza mwana wa tsiku limodzi akuyandama mumtsinje wa Lilongwe.
Iwo anati ana omwe ankasambira mumtsinjewo ndi omwe anapeza mwanayo ndipo anauza anthu ena, omwe anakafotokozera apolisi a ku Kanengo.
Mtseteka wati kafukufuku wa apolisi wasonyeza kuti Lyson anali ndi pakati pa miyezi yoposera isanu ndipo pa 31 October 2026 anayamba kuona zizindikiro zofuna kubereka.
Lyson anaitanitsa mnansi wake, Chotsani, komanso agogo ake aakazi, Santhe, kuti amuthandize pobereka.
Apolisi ati mwanayo atabadwa, amayiwa anapeza kuti wamwalira ndipo anagwirizana kubisa nkhaniyi chifukwa panalibe mwamuna amene akanatenga udindo pa mwanayo zomwe zinapangitsa kuti amponye mumtsinje wa Lilongwe.
Lyson anauza apolisi kuti amayi awiri achikulirewo ndi omwe anamulangiza kuti amuponye mwanayo mumtsinjewo ponena kuti mwamuna yemwe ankamuganizira kuti ndi yemwe anamupatsa mimba anali ataikana kale.