Apolisi ku Chikwawa atsimikidza kuti Maxwell Nsomera wa zaka 24, wafa gulu la amai ogulitsa matupi litamumenya pambuyo pa mkangano womwe unabuka ku malo ogona alendo a Tiyamike Rest house ku Nchalo.
Wofalitsa nkhani za apolisi ku Chikwawa a Dickson Matemba ati a Nsomera lolemba lapitali nthawi ya 2 koloko m’mbandakucha akubwelera kunyumba kuchokera ku mowa analowa m’nyumba yogona alendoyi.
Matemba wati malemuwa adapeza zipinda zonse zogona alendo zili zodzaza ndi amai ogulitsa matupiwa ali ndi makasitomala awo zomwe sizinamisangalase Nsomera.
Pamenepa Nsomera anayamba kulalatira makasitomalawo zomwe sizinasangalatse amai ogulitsa matupiwa omwe anamumenya mpaka kumukomola pambuyo pokangana ndi m’modzi mwa iwo, amai enawo asanalowelere.
Matemba anati anthu akufuna kwabwino anamtengera Nsomera ku chipatala cha Montfort komwe achipatala anatsimikiza kuti wafa kamba kovulala kwambiri m’mutu.
Malinga ndi Matemba, Apolisi akusakasaka anthu omwe akuganiziridwa kuti ndi omwe achita izi ndipo akamangidwa, adzayankha mlandu wakupha.




