Phungu wa chipani cholamula cha DPP m’dera la Rumphi West, Hon. Jonah Dada Wiza Mkandawire, MP, wachenjeza chipani cha DPP pa nkhani yokhudza chitukuko komanso chisankho cha mchaka cha 2030 ngati chipanichi sichikwanitsa malonjezo ake kwa a Malawi .
Wolemekezeka a Mkandawire ati nthawi yakwana tsopano kuti chipanichi chiyambe kuyala maziko a chitukuko chifukwa masiku akuthera ku chitseko.
Iye wati Amalawi akuyenera kuyamba kuona chitukuko chooneka ndi maso.
“Chonde akuluakulu, 2030 sikutali. Tiyeni tiyambe kuyala zitukuko paliponse. Tisabwereze zomwe amachita a MCP. Ngati tiyika zitukuko, mu 2030 sizidzafunika kuti tigule ma T-shirt kapena maheu, olo kugawa ndalama kwa mafumu, koma kungoloza zomwe tachita,” watero Mkandawire.
Phunguyu, polankhula, anadzudzula chipani cha MCP ponena kuti chinalephera kugwiritsa ntchito bwino ndalama zogulira maheu, zomwe akanatha kugwiritsa ntchito pomanga zipatala komanso masukulu.