Nduna yowona za maphunziro, sayansi ndi luso a Bright Msaka ati undunawu ukulemba aphunzitsi okwana 1,100 telemu yomwe ili mkatiyi.
Ndunayi yanena izi pomwe dziko lapansi lero likukumbukira tsiku la aphunzitsi ndipo yati kulemba ntchito aphunzitsi ndi mbali imodzi yopititsa patsogolo kagwilidwe ntchito kabwino ka aphunzitsi.
“Kuti maphunziro akhale apamwamba pamafunika kuti aphunzitsi akhale osulidwa bwino, okonzeka kugwila ntchito ndipo tikunena kuti aphunzitsi ndi mbali imodzi ya chitukuko,” atero a Msaka.
Ndunayi yapemphanso makolo, aphunzitsi ndi onse okhuzidwa pa nkhani za maphunziro kuti athandize kuzindikira zakufunikira kwa aphunzitsi.




