
Ku Dowa, m’busa wa mpingo wa Hope Ministries wapezeka atafa m’mawa wa lero atadzimangirira m’mudzi wa Thendo m’dera la mfumu yayikulu Mponela m’bomali.
Nyakwawa Thendo yati m’busayo, a Yosofat Amosi anawuza mwana wawo utsiku wadzulo kuti sakulandira malipiro kuntchito kwawo, ndipo akulephera kubweza ngongole zomwe ali nazo.
Iwo ati pakati pa usiku bamboyo anatuluka m’nyumba ponena kuti akukazithandiza koma sanabwereko kufikira lero m’mawa pomwe amupeza atafa.
Zotsatira zakuchipatala zikusonyeza kuti m’busayo wafa, kaamba kobanika. Pakadali pano apolisi sanayankhulepo pankhaniyi.



