
Timu yampira wamiyendo ya dziko lino ya osewera osapitilira zaka 23 yagonja 1-0 masewero ake ndi timu ya anyamata osapitilira zaka 23 a timu ya Eswatini pa bwalo la Bingu ku Lilongwe.
Awa ndi masewero odzipezera malo ku mpikisano wa maiko amu Africa wa osewera ake osadutsa zaka 23 a CAF U23 African Cup Qualifiers.
Malawi U23 inali ndi mipata yochuluka mzigawo zonse koma inalephera kupeza chigoli mpaka kumapeto a masewerowo.
Ngakhale mphunzitsi wa timu ya dziko linoyi Bob Mpinganjira anasintha ena mwa osewera koma sizinaphule kanthu.
Malawi U23 ikuyenera kukapambana masewero achibwereza ku Eswatini mmasiku akudzawa ndi zigoli zosachepela ziwiri kwachilowere kuti ipitilire mu mpikisanowu.
Opambana pa masewero awiriwa adzakumana ndi timu ya Algeria U23.




