
Bambo wina a Chikondi Mavuto a zaka 21 apezeka atafa kutchire atamwa poizoni m’boma la Machinga.
Malingana ndi Ofalitsa nkhani za Polisi m’boma la Machinga a Western Kansire anthu anapeza thupi la a Mavuto pa 4 September 2026 nthawi ya 6 koloko mamawa mmudzi mwa a Masaka m’bomali.
Kansire wati a Mavuto anamubwereka mchimwene wawo K50,000 ndipo malemuwa samabwezeredwa ndaalamayo ngakhale amakakumbusa zangongoleyo pafupipafupi.
“Pa 1 September malemuwa anapitanso kwa mchimwene wawo kokumbutsa ndalamayo ndipo awiriwa anakangana kwambiri. Izi zinapangitsa a Mavuto kudandaulira mzawo wapamtima za khalidwe la mchimwene wawo komanso lingaliro lawo lofuna kuzipha,” watero Kansire.
Pa 4 September ndipamene a Mavuto anapezeka atamwalira komanso thupi lawo linali litaonongekaratu popeza linali litapsanso ndi moto wa mtchire ndipo azimayi omwe amasaka nkhuni ndi amene anapeza thupi la malemuwa.
A Polisi ya Ntaja komanso akadaulo azachipatala atathamangira kumalo angoziwo ndipo atachita kafukufuku apeza zoti imfa ya malemuwo inaza kaamba kakumwa poizoni.
Apa apolisi apempha anthu kuti azipempha uphungu ku Polisi ndi malo ena oyenera akakhala kuti akumana ndi mavuto mmoyo wawo
A chikondi Mavuto anali ochokera mmudzi mwa Masaka , Mfumu yaikulu Liwonde, m’boma lomweli la Machinga.
Chithunzii ndi cha AI generated