
Mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) komanso mtsogoleri wakale wa dziko lino, Dr. Lazarus Chakwera, wanena kuti anthu ena m’chipanichi ndi amene anathandizira kuti chipanicho chigonje pa chisankho cha chaka cha 2025.
Polankhula ndi otsatira chipanichi ku Chileka mumzinda wa Blantyre, Chakwera adati ena mwa nduna m’boma lake lakale sankagwira ntchito mogwirizana, zomwe zinkasokoneza mgwirizano m’boma.
Iye adati ngakhale MCP inali m’boma, atsogoleri ena ankatsatira zofuna zawo m’malo mogwira ntchito limodzi pokwaniritsa zolinga za chipanicho.
“Tidali m’boma tokhatokha, tinayamba kuonana mosiyana. Aliyense ankangolimbikitsa zakezake. Anthu anachulukitsa individualism osati teamwork,” adatero Chakwera.
Mtsogoleriyu adanenanso kuti chifukwa cha khalidwe lodzikundikira komanso kusagwirizana kumeneku, anthu ena masiku ano akumunyoza.
“Ena lero chifukwa cha mtima umenewu, chifukwa chodzikundikira, akunena kuti Chakwera ndi chitsiru,” adatero.
Chakwera adati waphunzira zambiri kuyambira pomwe adachoka pa udindo wa pulezidenti, ndipo watsindika kuti anthu amene akulimbana naye akungowononga nthawi yawo.
Iye adadzudzulanso boma lomwe lilipo pakadali pano, ponena kuti likuchotsa masomphenya a chitukuko omwe boma lake linali litakhazikitsa.
Pomaliza, Chakwera adanenetsa kuti ali ndi ufulu wokhala ndi kutumikira m’dziko lake, ndipo palibe amene angamulepheretse kutero.
“Ine kuno ndi kwathu, palibe amene angandilembere malire,” adatero.



