
Apolisi m’boma la Kasungu atsimikiza za imfa ya a Mustafa Nthandi azaka 39, omwe amaganizilidwa kuti anaba katundu pa malo a ntchito, ndipo afa pozimangilira ali m’chitokosi cha apolisi.
Malinga ndi woyankhulira apolisi m’chigawo chapakati chakummawa, Esther Mkwanda, izi zachitika lero ku mmawaku pomwe a Nthandi anapemba kuti akazithandize.
Mkwanda wati Nthandi yemwe amachokera mdera la Chilanga, mfumu yaikulu Kaomba m’boma lomweli anagwiritsa ntchito malaya omwe anavala pozimangilira.