
Mpingo wa Seventh Day Adventist m’dziko muno kudzera mwa mtsogoleri wake m’busa Petros Sukali komanso mkulu wa chipatala cha Blantyre Adventist Hospital apempha nduna ya zaumoyo a Madalitso Baloyi kuti athandizirepo pa vuto la kuzima kwa magetsi pa chipatalapa.
Iwo ati pena magetsi amazima kwa maola 9 pachipatalapa, zomwe zikumasokoneza ntchito yothandiza odwala ndi kuika miyoyo yawo pachiopsezo.
Akuluakulu awiriwa ayankhula izi pa mwambo wotsegulira ntchito yomanga chipatala chopanga opaleshoni ya mtima chomwe chikhale choyamba m’dziko muno.
Mwini wake wa Banki ya FCB a Hitesh Anadkat ndi omwe athandize ndi ndalama zokwana $3 million (pafupifupi K5.3 billion) zogwirira ntchitoyi.