
Bwalo la mlandu ku Monkey Bay lagamula anyamata awiri Exvin Nangwale wazaka 21 ndi Patrick Saphika wazaka 20 kuti akakhale ku ndende kwa zaka khumi (10) komanso zisanu (5) aliyense kaamba kozembetsa mwana wina yemwe ankafuna amugulitse m’mudzi wa Ntemwende m’boma la Mangochi.
Lyson Kachikondo amene amayimila boma pa mulanduwu anauza bwalo la milandu la Monkey Bay lero kuti anyamatawa anamangidwa pa 12 September chaka chino, pamene a polisi anatsinidwa khutu ndi anthu akufuna kwabwino kuti awiriwa amasunga mwana ndipo amasaka munthu oti awagule mwanayo.
Malingana ndi a Kachikondo, Patrick Saphika ochokera m’mudzi wa Dickson, mfumu yaikulu Nankumba ndi amene anapeza msika pamene Exvin Nangwale amachokera m’mudzi wa Kaiche kwa Nankumba komweko.
Popeleka chigamulo chake, oweruza milandu a Roy Kakutu wagamula Saphika kukakhala ku ndende kwa zaka khumi, pamene Nangwale amupatsa zaka zisanu.



