Ku Dowa apolisi amanga m’busa Medran Chirwa wa mpingo wa Fountain of Victory Church ku Lilongwe pomuganizira kuti akukhudzidwa ndi imfa ya a Tathokoza Salimu, omwe anapezeka atafa mu galimoto ina m’bomali.
Malemu Tathokoza amagwira ntchito ku banki ya FDH ndipo anapezeka atafa pa 21 September 2026 anthu ena atawapeza malemuwo pafupi ndi mlatho wa Tatolonga msewu wopita ku Dzaleka.
Malingana ndi Alice Sitima wofalitsa nkhani za apolisi ku Dowa, zokambirana za pa foni ya malemu Tathokoza zikusonyeza kuti patsiku lomwe anachitidwa chiwembucho, anali limodzi ndi a Bishop Medran Chirwa




