
Mtsogoleri wa dziko lino professor Arthur Peter Mutharika wachotsa a Joseph Bongololo Gondwe ngati Mfumu Yaikulu Chikulamayembe (Paramount Chief).
Reverend Moses Chimphepo mlembi wamkulu mu unduna wa maboma ang’onoang’ono wati izi zikutsatira dadandaulo kuchokera kwa omwe ufumuwu umachokera.
Chimphepo ati a Joseph Bongololo Gondwe anasankhidwa potsatsata ndondomeko ya mlowam’malo ku chikhalidwe cha a Tumbuka kunena kuti ndondomeko zimanena kuti mwana ndi amene amayenera kutenga ufumu.
Apa mlembi wa mu undunawuyu wapempha a Gondwe kuti aonetsetse kuti pali mgwilizano pomwe ufumuwu ukhale ukubwelera kwa munthu mlowam’malo oyenera.
A Bongololo Gondwe anakhazikitsidwa ngati Paramount Chief mchaka cha 2022 ndi mtsogoleri wakale wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera.



