
Mwambo wa mapemphero wosikana ndi a Carver Bhima yemwe anali kaswiri pokonza mpikisano wa ziphadzuwa za dziko lino uli mkati pa tchalitchi ya Holy Innocents ku Limbe munzinda wa Blantyre.
Mwambowu ukatha thupi la malemuwa alitengera ku nyumba kwawo ku Chigumula mumzindq womwe uno wa Blantyre pokonzekera mwambo wa maliro womwe uchitike mawa lachisanu.
Cha ku mmawaku anthu ambiri anasonkhana ku Kamuzu University of Health Sciences (KUHES) komwe amanyamula thupi la malemuwa.
A Bhima omwe anali ndi zaka 85 anamwalira lachiwiri sabata ino atadwala nthenda ya mtima ndipo anali mmodzi mwa anthu amene anayambitsa mpikisano wa Ziphadzuwa za dziko lin.



