Sitima yapa madzi yotchedwa MV Mtendere yagwa ndipo ikumila padoko la Monkey Bay m’boma la Mangochi komwe yakhala ili chiyimile kwazaka pafupifupi khumi ndi chimodzi.
Akuluakulu a Kampani ya Malawi Lake Services yomwe imayang’anila dokoli ati ali mkati mochita kafukufuku wokhudza chomwe chachititsa kuti sitimayi yomwe idakocheza pa doko la Monkey Bay itasiya kugwira ntchito zake kwa zaka zochuluka itembenuzike ndi kumila.
Mmodzi mwa ogwira ntchito ku Malawi Lake Services wati pambali pa kafukufuku-yu pali mphekesera zakuti anthu ena omwe akuganizilidwa kuti amafuna kuba zinthu Zina mkati mwa sitimayi ndi omwe achititsa izi atatsegula Malo ena omwe analowetsa madzi mu sitimayi.
Malingana ndi zomwe tapeza akuti Sitimayi inayamba kumila m’bandakucha wa lero ndipo m’mene imakwana 4 koloko mawa walero inali itagwera m’madzi mbali imodzi
Iwo ati kutembenuzika kwa sitimayi sikukubweretsa chisokonezo chilichonse ku ntchito za kampaniyi koma adzudzula mchitidwe wa kubawu ponena kuti kampaniyi iwononga chuma chambiri kuti ibwezeretse sitimayi mmalo mwake .
izi zikuchitika sitima ya MV mtendere itasiya kugwira ntchito zake pa nyanja ya Malawi kwa zaka zochuluka tsopano pamene akuti inayenda ulendo wake wapamadzi omaliza mu zaka za pakati pa 2012 ndi 2013, kenako inayimitsidwa pofuna kuti ikonzedwe kaye.




