
Pulezidenti wachisanu ndi chimodzi wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera akuyembekezereka kukhala nawo pa mwambo oyika mmanda thupi la malemu Zimani Kadzamila amene anamwalira lachisanu lapitali.
Malingana ndi chikalata chomwe wasayinila mneneri wa mtsogoleri wakaleyu a Gift Nankhuni Dr Chakwera apita ku mwambowu pamodzi ndi mayi wakale wafuko lino a Monica Chakwera.
A Chakwera akuyembekezeleka kufika ku mwambowu womwe uchitikile ku Linthipe , m’boma la Dedza nthawi ya 9 koloko mamawa.
Professor Zimani Kadzamila adali kaswiri wazamaphunziro ndi adakhalapo wachiwiri kwa Mkulu wa Sukulu ya Ukachenjede ya Malawi komanso adali mchimwene wawo wa mayi Cecilia Kadzamila.



