
Bwalo la Chief Resident Magistrate ku Blantyre lapeza nzika ya m’dziko la Netherlands Wim Akster olakwa pa milandu isanu yokhudza kugonana ndi anyamata achichepere ndipo bwaloli lizapeleka chigamulo chake pa 01 December 2026.
Chigamulochi chabwera, oweruza ku bwaloli Chief Resident Magistrate ataunikira maumboni a mbali zonse ziwiri.
A Akster adamangidwa powaganizira kuti amachita mchitidwe ogonana ndi anyamata omwe amafuna thandizo la maphunziro ku bungwe la Timotheos Foundation pakati pa 2019 ndi 2020.
Padakali pano bwalo la milanduyi lawachotsera belo a Akster, ndipo akhala akusungidwa ndende kufikila tsiku la chigamulo pa 01 December mwenzi ukudzawu.
Mmawu ake oyimira boma pa milandu Victor Jere wati ndiokondwa kuti tsopano mulanduwu wakomera mbali yawo utakhala ku bwaloli kwa zaka zisanu ndi chimodzi (6).
Naye omenyera ufulu wa ana Memory Ngosi wayamikira bwaloli poonetsetsa kuti chilungamo chadziwika pa mulanduwu.