
Bungwe lowona za malonda a fodya la Tobacco Commission lati dziko lino lapeza ndalama zokwana $286.1 miliyoni kuchokera ku makilogiramu 144.5 miliyoni amene agulisidwa munyengo yogulitsa fodya ya chaka chino.
Bungwe la Tobacco Commission lanena izi pamene msika wa fodya watsekedwa patatha masabata makumi awiri ndi imodzi dziko lino likugulitsa fodya malo amene mbewuyi imagulitsidwira.
Msika wa fodya chaka chino unakumana ndi mavuto akuchuluka kwa mlingo wa fodya ameme alimi analima poyelekeza ndi mlingo umene ogula fodya amafuna zimene mwazina zinapangitsa kuti fodya wambiri azibwezedwa pamsika wa Auction.
Msika wa fodya wachaka chino unasegulira pa 20 April 2026.