
Patangotha mwenzi umodzi sitima ya MV Chambo ya dziko la Mozambique itayaka moto pa nyanja ya Malawi Kampani kampani yoyang’anira sitima ndi mayendedwe apa Nyanja ya Malawi Lake Services yaletsa anthu kunyamula mowa wa kachaso ndi zinthu zina zilizonse za madzimadzi muzigubu mu Sitima ya MV Ilala.
Malingana ndi Mkulu wa Kampaniyi a Joseph Banda chiletsochi chikudza kaamba koti Lachisanu pa 6 November 2026, pamene Sitima ya MV Ilala imayamba ulendo wake kuchokera ku Monkey Bay anthu ena anakweza zigubu zomwe amati munali mowa wa Kachaso, koma mwa zigubuzi munapezeka china choti chinali ndi mafuta a Petulo.
Joseph Banda nda wati chigubu chamafutacho chinabooka mpaka mafuta anayamba kuyendelera kufika m’ma Cabin ena zomwe ati ndi zopereka chiopsezo kwa anthu okwera sitimayi chifukwa zitha kuyambitsa moto ponena kuti anthu ena amapezeka akusuta fodya ali paulendowu zomwenso ndi zosaloledwa.
Iye wachenjeza onse omwe amanyamula mowa mzigubu ndikumakwera Sitimayi kuti nthawi yawo yatha ndipo kuyambira pano anthu onse onyamula mowa kapena mafuta mzigubu azipeza ma boat a padera oti aziwanyamulira katunduyu kupita ku madera osiyanasiyana.