
Pamene dziko lino likuyembekezeleka kukumana ndi nyengo ya El Niño mu nyengo ino ya dzinja dziko la China lalonjeza zopereka mpunga wa matani okwana 1,892 a ndalama zokwana 3 million dollars (pafupifupi 5.2 billion kwacha) ku dziko la Malawi.
Dziko la China lalengeza izi kudzera pa lake lamchedzo la Facebook ya Kazembe wa dziko la China mdziko muno ndipo uthengawu wati mgwirizano wa thandizoli usainidwa posachedwapa.
Dziko la China lati thandizolo likuonetsa kudzipereka kwa dzikolo pothandiza dziko la Malawi pomwe likukhudzidwa ndi mavuto a El nino ndipo likuchilimika pofuna kuthana ndi mavuto a njala.