
Khonsolo ya boma la Mwanza lati nthambi yoona zangozi zogwa mwazizizi ya DoDMA ndiyo ikuyenera kukonza bwalo lazamasewero la Joyce Chitsulo kuti lifikenso pa mlingo woti itha kuyamba kugwiritsidwa ntchito m’masewero osiyanasiyana.
Malingana ndi bwanankubwa waboma la Mwanza a January Mvula, nthambi ya boma yoona za ngozi zogwa mwadzidzi ndiyomwe ikuyenera kukonza bwaloli osati khonsolo ya Mwanza
Anthu okonda masewera osiyanasiyana a m’boma la Mwanza akuyenera kupilira ndi kudekha poyembekezera tsiku lomwe bwalo la Joyce Chitsulo lidzatsekulidwenso.
Mvula wafotokoza izi pamene anthu ena m’bomali akupempha khonsoloyi kuti igwiritse ntchito gawo lina la ndalama za CDF kukonzera bwaloli.
Bwanamkubwayu wati pali zambiri zofuna kukonzedwa bwaloli lisanatsekulidwenso kwa anthu kuti adzipangapo masewero osiyanasiyana.
Bwalo la Joyce Chitsulo linaonongeka panthawi yomwe boma kudzera ku Bungwe la DoDMA linkalandira mzika za dziko lino zomwe zinkathawa zipolowe zodana ndi mzika zobwera ku South Africa.
Achinyamata komanso anthu okonda masewero osiyanasiyana a m’boma la Mwanza akuvutika pankhani yaza masewero chifukwa chakutsekedwa kwa bwali.