Apolisi ku Mangochi amanga anthu atatu amene anali mgulu la a Malawi omwe abwera miyezi itatu yapitayi kuchokera ku South Africa powaganizira kuti athyola mu sitolo ina ndikuba mabulangete andalama zokwana K2.7 miliyoni.
Malingana ndi wofalisa nkhani za Polisi ya Mangochi a Amina Tepani Daudi amuna atatuwo ndi Kaisi Jalasi a zaka 34, Watson Mtuwa a zaka40, komanso Muhammad James a zaka 24.
Anthuwa akuwaganizira kuti anathyola sitolo ya a Shakira Mussa, usiku wapa 19 October 2026.
M’mawa wapa 20 October, Mussah analindira uthenga kuti sitolo yake yathyoledwa ndipo atafika pamalopo, anapeza kuti mabulangete okwana 25 atsopano abedwa ndipo nthawi yomweyo anapereka lipoti ku polisi.
Daudii wati a polisi anayamba kafukufuku pa nkhaniyi ndipo anakwanitsa kugwila anthu atatuwa komanso kupeza mabulangete onse 25 omwe anabedwawo.
Pakafukufukuyu, apolisi anapezaso zida zosiyanasiyana zomwe zinali zobisidwa ndipo apolisi akuganiza kuti ndizomwe anthuwa ankagwilitsa ntchito pofuna kuthyola nyumba ndi sitolo.
Jalasi amachokera m’mudzi mwa Kwisimba, Mfumu yaikulu Katuli, pamene Mtuwa ndi James amachokera m’mudzi mwa M’baluku, Mfumu yaikulu Chowe m’boma la Mangochi.
Abambo atatuwa akuyembekezeka kukawonekela ku bwalo la milandu kuti akayankhe milandu yothyola nyumba ndi kuba, apolisi akadzamaliza kufufuza kwawo.




