
Bungwe la Admarc latsimikizira Amalawi kuti asade nkhawa kaamba koti lili ndi chimanga chokwanira 9000 metric tonnes m’misika yake ndi 3000 metric tonnes mu nkhokwe zake pomwe bungwe la National Food Reserve Agency (NFRA) likupitilira kugula chimanga.
Mmodzi wa ma mamembala a board ya bungweli a Grey Kapute anena izi kwa atolankhani lero pamene akuluakulu ena a bungweli amayendera ma depot a Admarc m’maboma a Chikwawa ndi Nsanje kumene Amalawi akugula chimanga pa mtengo wa K1000 pa kilogilamu.
Iye anatinso ADMARC ili ndimalingaliro ofuna kugula masikelo a digito pafupifupi 300 kuti akalowe m’malo mwa akale omwe ali m’misika ndi m’ma depot ake.
Kapute wati bungwe la Admarc liyesetsa kuti chimanga chizipezekabe m’misika yake pamene NFRA ikupitilira kugula chimanga kugwiritsa ntchito ndalama zokwana K100 billion zimene inapasidwa.
Dziko la Malawi likuyembekezeka kukumana ndi nyengo ya El Nino munyengo ino ya mvula zimene zitha kubweretsa ng’amba yomwenso itha kusokoneza zokolola chaka cha mawa.