
Chaka chino ogwira ntchito m’boma ayamba tchuthi chawo cha Christmas komanso chaka chatsopano pa 14 December 2026 mpaka pa 01 January 2027.
Malingana ndi chikalata chomwe wasayinila ndi Mlembi wamkulu wa boma Dr. Justin Saidi, ogwira ntchito m’boma adzayambanso kugwira ntchito yawo lolemba pa 04 January 2027.
Said wati tchuthichi, chipeleka mpata kwa ogwira ntchito m’boma kuti apume komanso kuyendera malo osiyanasiyana pa nthawi ya chikondwelelochi.
Koma chikalatachi chati ofesi zina monga ku polisi, immigration komanso ku chipatala zikuyembekezeka kudzagwirabe ntchito pa nthawiyi.