
Mkulu wina yemwe ndi nzika ya ku Burundi yodziwika a Minanie Batazare apha mkazi wawo Hekizimana Coillinie poyatsa nyumba yawo kenako ndikuzipha pokumwa mankhwala ambewu kumsasa wa Dzaleka ku Dowa.
Malingana ndi m’neneri wa polisi ya Dowa Alice Sitima a Batazare achita izi dzulo ndipo anayatsa nyumbayi mkazi wawo ali mnyumba mommo.
Sitima wati mkulu wa ku Burundiyu anadziwitsa mchimwene wake za malingaliro ofuna kuyatsa nyumba yake ndipo achimwene akewo anathamangile kunyumbayo koma pomwe amafika anapeza mkazi wa achimwene awo atafa.
Iwo ati thupi la a Batazare linapezeka kufupi ndi manda ena m’bomali ndipo atathamangura nawo ku chipatala, achipatala anatsimikiza kuti anali atafa kale.
Pakadali apolisi ati cholinga chomwe a Batazare achitira izi sichinadziwike.



