Bwalo la Supreme ku Blantyre lakana pempho la a Yeremiah Chihana amene anali mkulu wa Blantyre Water Board kuti liyimitse chiganizo cha akulukulu a bungweli, chowayimitsa pa ntchito, komanso kuti liwunikenso chiganizocho.
Mosogozedwa ndindi wachiwiri kwa mkulu wa mabwalo a milandu a Lovemore Chikopa ndi oweruza ena asanu ndi mmodzi agwirizana ndi mbali ya boma kuti nkhani ya a Chihana ikuyenera kumvedwa ndi bwalo la Industrial Relations, komanso panali zolakwika pa pempho lawo.
Mkulu oyimira boma pa milandu a Frank Mbeta, anauza bwalo kuti pempho la a Chihana linalibe zifukwa zokwanira.
Izi zikutanthauza kuti a Chihana sakuyenera kubweleranso ku ntchito yawo ngati mkulu wa Blantyre Water Board.




