Mkulu wa a Polisi M’ dziko muno a Richard Luhanga wapeleka K1 miliyoni komanso kukweza udindo apolisi asanu ndi atatu amene anathandizira kupulumutsa a Nusrat Osman nzika ya ku Britain.
A polisi asanu ndi atatuwa ndi amene anagwira ntchito ndi a Noel Kaira Wachiwiri kwa Mkulu wa Polisi m’dziko muno populumutsa nzika ya ku Britain yi yomwe inagwidwa ndikumasungidwa mokakamiza ndi anthu ambanda ena ku Mount Pleasant mu Mzinda wa Blantyre masiku angapo apitawa.
Mneneri wa Polisi m’dziko muno a Gladys Chiwaula atsimikiza za nkhaniyi ponena kuti a Polisi asanu ndi atatuwa atsonyeza kudzipeleka pa ntchito yawo n’chifukwa chake awakweza ma udindo awo.




