
Apolisi ku Luchenza M’boma la Thyolo amanga bambo wazaka 27 a Chisomo Andrew pomuganizila kuti wagwilira mwana wamkazi wazaka zinayi M’bomali.
Malingana ndi Wofalisa Nkhani za Polisi ku Luchenza a Baseke Mwale a Chisomo anachita izi ku manda otchedwa Manda a Alendo ndipo anthu ena amane amasamba mu mtsinje wa Thuchila ndamene adamva kulira kwa mwana mmandamo.
Apa anthuwo anathamangirako ndipo adapeza mkuluyo akuchita zosayenera ndi mwanayo ndipo adamugwira ndikupita naye ku Polisi.
Zosatira zakichipatala zasonyeza kuti mkuluyo adagonadi ndi mwanayo ndipo pakadali pano mwanayo akulandira thandizo lachipatala.
Chisomo Andrew amachokera Mudzi mwa Ndalama mdera la Mfumu yaikulu Mchiramwera M’boma lomwelo la Thyolo.



