Msundwe barracks under Malawi Congress Party militia wing who have been eloped into Malawi Congress Police have shot dead Asidi Sumbeja, a driver for a 1.5 tonne pickup truck in Zomba .This publication can reveal he is an in law to MCP’ Richard Chimwendo Banda .
Malawi Police under the leadership of Chikangawa Chakwera as commander in Chief and Kamajekete Zikhale Ng’omba as minister of homeland security has turned into the country into a police state .
This is what our publication has established reported by Times 360.
Pali mphekesela zoti apolisi awombera mkupheratu dalaiva wina pa road block ya 4 miles ku zomba.
Malingana ndi wachiwiri kugulu la oyendetsa ma taxi a 3 miles -Chinamwali rank, a Asidi Sumbeja wati dalaivayo yemwe dzina lake ndi Zakeyu Matekenya amayendetsa galimoto la 1.5 ton kuchoka k Thondwe kumalowera mbali ya mtown ya Zomba ndipo ananyamula anthu ogulitsa mabelo.
Iwo atafika pa 6 miles iwo anaimisidwa ndi a polisi a speed trap koma sanaime ndipo dalaivayo anatchingilidwa nsewu ndi apolisi apa road block ya 4 miles omwe ati anaombera teyala la galimotolo komanso kuombera dalaiva kumsana.
“Apapa tili ku motchale komwe tikulondoloza nkhaniyi koma ndithu nzathuyu wamwalira,” anafotokoza a Sumbeja.
Mmeneri wa chipatala cha Zomba, a Fredson Kambeni ati kuchipatalaku alandiradi thupi la munthu omwe waombeledwa ndi mfuti ndipo anafika naye atamwalira kale.
Mmeneri wa apolisi mchigawo chakummawa a Patrick Mussa anati sangayankuleko kaye pankhaniyi pomwe nawo ali mkati mofufuza zomwe zachitika.
Dalaiva wina watiuza kuti pano anthu amudzi omwe anaona izi zikuchitika atseka nsewu ndipo apolisi omwe akuthira utsi okhetsa misozi afika pamalopo ndipo galimoto zopita ku Blantyre kuchoka ku Zomba sizikudutsa.
Tipitilire kukupatsirani zambiri pa nkhaniyi.