Dzulo, ana atatu paubale wawo a kwa Sale ku Machinga analowa mtchire kukasaka chilichonse choti adye kutsatira njala imene akumaswera nkugona nayo kwa masiku ambirimbiri. Kutchireko anapeza zipatso za mtengo wa Mkweranyani zimene anatchola nkudya kuti mwina aponyemo kenakake m’mimba.
Koma onse atatu atangodya anakomoka komweko.
Anthu kumudzi atamva anathamangira nawo kuchipatala koma asanafike, m’modzi mwa anawo wamwalira ndipo awiriwo pakadali pano adakali chidwalire mwakayakaya.
Machinga needs saving!
https://youtu.be/iyz00la1loI?si=MrphrZe4nhjdgRbp
https://youtu.be/079Lf8z-88Y?si=8m1IM9aarLW9Cn87