A Polisi ya Ndirande mu mzinda wa Blantyre ati anthu okwana 7 ndi omwe amwalira pa ngozi imene yachitika mu msewu wa Magalasi chaku madzuloku.
Anthuwa amachokera ku bwalo la masewero la Kamuzu kumene adakalandira chimanga chimene bungwe la Dodma likupereka kwa anthu.
Malinga ndi wofalitsa nkhani pa polisi ya Ndirande a Maxwell Jailosi, galimotoyi idanyamula anthu okwana 37 ndipo mwa anthuwa awiri ndi amene avulala modetsa nkhawa pamene asanu awathandiza ndipo awatulutsa.
Galimoto ya mtundu wa lorry limene anthuwa adakwera, malinga ndi amene adaona izi zikuchitika a Isaac Chilenje, lidaonongeka mabuleki zimene zidachititsa kuti lithamange kwambiri lisadagwe.