Times360Malawi
A Kabambe omwe apeleka cheke cha K20 million ati nthumwi zikawavotere chifukwa iwo all ndi ukadaulo oyendetsa chuma cha chipani komanso cha dziko.
A Kabambe omwe anali mkulu wa banki yaikulu ya dziko lino ati boma lomwe lilipo pakadali pano lalephera kuyendetsa chuma cha dziko.
“Panopa osauka akusaukirabe, anthu alibe chakudya. Mvulanso yayamba koma alibe feteleza. Omwe ali ndi galimoto ndiye akugona mma filling station nawo mavuto okhaokha. This government is clueless, it doesn’t know a anything and that’s why they say running government is not for babies,” atero a Kabambe.
A Kabambe, atinnso anthu mu chipani cha UTM abwere pamodzi ndikupanga kampeni yovuta kuti chaka cha mawa atenge boma.
“Amalawi ayesapo zipani zina, zalephera. Pano yesani UTM. Ine Dalitso Kabambe lero ndapeleka zikalata zosonyeza chidwi kupikisana, ndili ndi ukadaulo oyendetsa chuma cha dziko ndipo zinthu zambiri zomwe boma ili likupanga molakwikwa, mayankho ake ndili nawo,” atero a Kabambe.