Two people have passed on in Blantyre after eating natural roots which were looking like cassava. This follows lack of maize and food for most of Malawians under Malawi Congress Party regime who have resorted to eating dangerous and poisonous herbs .
Ana awiri omwe ndi abanja limodzi afa komanso ena awiri adakali m’chipatala atadya zinthu zooneka ngati chinangwa m’mudzi mwa achisinga ku machinjiri m’boma la Blantyre.
Malingana ndi amalume awo a anawa a Alfred Manondo ati anawa omwe wina ndi wadzaka zosachepera 6 ndipo wina wadzaka zisanu anachoka kukasaka chakudya chifukwa cha njara, ndipo anapeza Munda wina omwe anadzula zinthu zooneka ngati chinangwa kuti akadye ngati chakudya chawo cha madzuro, ndipo atadya pomwe anayamba kusanza ndikutsekula m’mimba ndipo anathamangira nawo ku chipatala.
Mkulu wa polisi ya south Lunzu a Patricia Jawiri watsimikiza kuti anawa afa atadya chinangwa.
Wolemba Agness Mpulula ndi Cynthia Mpofu
Welengani zambiri pa Kanema M’manja
Download Kanema M’manja NOW on playstore to watch and catchup all your favaourite programs.
https://play.google.com/store/apps/details?id=com.mibawa_studios.mibawa_tv&fbclid=IwAR0J2FYp09NRYBp43uNa7znE0KArPlufqrK4_Oks5XlbFN0KhtTfiHnth-o