
Ngati mukufuna kulembetsa ukwati wanu ku khonsolo ya Blantyre mukuyenela sopano kukonzekela bwino pamene khonsoloyi yalenegeza kuti yakweza mtengo wa ndalama wolembetsera ukwati wa aMalawi okhaokha kuchoka pa K30,000 kufika pa K80,000.
M’neneri wa khonsoloyi a Kondwani Chisi wati mitengo yawo inali yotsika kwambiri poyelekeza ndi kwina.
Iye wati mtengo wa ukwati okhudza nzika ya dziko lino ndi nzika ya dziko lina wafika pa K250,000.
Malingana ndi Chisi mapepala a ukwati ndi ofunikila kwambili ndipo ndizofunika kukhala nawo musanayambe kukhala limodzi ndipo banja likavuta amathandizira pogawa chuma ndikatundu.
“Tikupempha anthu kuti asamangoyamba kukhalira limodzi osapanga dongosolo koma azidzalembetsa ukwati wawo kwa DC. Pepala la ukwati limathandiza pogawa chuma komanso anthu akapeza ntchito kunja.” atero a Chisi.
Tiyeni a Malawi tikalembetse ma ukwati anthu kupangira pa mawa.