
Apolisi m’boma la Nkhotakota amanga anthu 71 amene akuganizilidwa kuti amakumba miyala ya mitengo wapatali mu nkhalango yotetezedwa ya Nkhotakota popanda zikalata zowayeneleza.
Malingana ndi Wofalitsa nkhani za polisi ya Nkhotakota Chisomo Chuma, mwa anthu 71 omwe awagwira 20 ndi ana osakwana zaka 18, pamene 4 ndi amayi ndipo izi zachitika mutsinje wa Likowa mkati mwa nkhalangoyi.
Chuma wati ntchito yogwira anthuwa anaigwira limodzi ndi alenje a nkhalangoyi.
Apa Chuma wati anthuwa ayankha milandu itatu yomwe ndi kulowa nkhalango yotetezedwa opanda chilolezo, kupezeka ndi zida komanso kukumba miyala ya mtengo wapatali opanda zikalata zowayeneleza.