
Ku Salima anthu awiri afa ndipo ena awiri avulala miyendo dzenje lomwe amakumbamo miyala ya mtengo wapatali litawagwera m’mphepete mwa Mtsinje wa Lipimbi m’bomalo.
Malingana ndi Wofalisa nkhani za Polisi ya Salima Rabecca Ndiwate anthu omwe amwalirawo ndi apachibale, a Sitaifodi Sailota azaka 26 ndi a Limbikani Sailota azaka 20 pamene a Benson Chrispin azaka 21 ndi Aubrey Malizan azaka 25 ndi omwe avulala miyendo pangozi-yi.
Ndiwate wati ngoziyi yachitika dzulo m’mudzi wa Bezai, m’dera la T/A Khombedza m’boma la Salima lo.
“Anthu anayiwa anathira madzi m’dzenje kuti nthaka ifewe ndipo kuti zikhale zosavuta kukumba. Mwadzidzidzi, khoma la dzenjelo linawagwera,” anatero Ndiwate.
Anthuwa anatengeredwa ku chipatala cha Makiyoni komwe achipatala anatsimikiza kuti a Sitaifodi ndi Limbikani amwalira kusatila kuvula komwe anavulala pa nthawi yangoziyo.



